1 Kings 20:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka musonkhanitse gulu lankhondo lofanafana ndi gulu lankhondo lidaonongeka lija, akavalo onga omwe aja, ndi magaleta onga omwe ajanso. Pambuyo pake tidzamenyana nawo ku chigwa. Ndithudi, pamenepo tidzaŵapambana.” Benihadadiyo adamvera mau a akuluakulu akewo, ndipo adachitadi momwemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magaleta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pachidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musonkhanitsenso gulu lankhondo lofanana ndi lomwe linaphedwa lija, akavalo monga omwe anaphedwa aja, ndi magaleta monga omwe anawonongedwa aja, kuti tikamenyane ndi Israeli ku chigwa. Pamenepo, ife tidzapambana iwowo.” Beni-Hadadi anagwirizana nawo ndipo anachita momwemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magareta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pacidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.