1 Kings 20:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Israele adasonkhana, ndipo atalandira zofunikira, adapita kukamenyana ndi Asiriya. Ndiye adamanga zithando zao zankhondo moyang'anana ndi Asiriya ndipo ankangooneka ngati timagulu tiŵiri ta mbuzi, m'menemo Asiriya adaadzaza dera lonselo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aisraele anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisraele anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta anaambuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli atasonkhananso, napatsidwa zakudya zawo anapita kukakumana nawo. Aisraeli anamanga misasa yawo moyangʼanana ndi Aaramu ndipo ankaoneka ngati timagulu tiwiri ta mbuzi, pomwe Aaramu anali atakuta dera lonselo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aisrayeli anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisrayeli anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta ana a mbuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.