1 Kings 20:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo nkuti anthu a ku Israele ndi a ku Siriya atakhala m'zithando moyang'anana masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku la chisanu ndi chiŵiri, nkhondo idagundika. Anthu a ku Israele adakantha Asiriya okwanira 100,000 tsiku limodzi lokha, ankhondo apansi okhaokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo awa anakhala m'misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israele anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa masiku asanu ndi awiri anakhala moyangʼanana mʼmisasa yawo, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri nkhondo inayambika. Aisraeli anapha Aaramu okwana 100,000 tsiku limodzi lokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo awa anakhala m'misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israyeli anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.