1 Kings 20:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena otsala adathaŵira ku mzinda wa Afeki, ndipo khoma lidagwa, kugwera pa anthu okwanira 27,000, omwe adatsalawo. Benihadadi nayenso adathaŵa, nakabisala m'chipinda cham'kati mumzindamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumudzi, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mudzi, m'chipinda cha m'katimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena onse otsala anathawira ku Afeki, kumene khoma linagwera anthu 27,000. Ndipo Beni-Hadadi anathawira mu mzinda, nakabisala mʼchipinda chamʼkati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumudzi, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mudzi, m'cipinda ca m'katimo.