1 Kings 20:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo akuluakulu ake adamuuza kuti, “Onani tsono, ife tamva kuti mafumu a fuko la anthu a ku Israele ngachifundo. Tiyeni tivale ziguduli m'chiwuno ndi kuzeŵeza zingwe m'khosi, tipite kwa mfumu ya ku Israeleyo, mwina sakakuphani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anyamata ake anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israele ndi mafumu achifundo; tiyeni tivale chiguduli m'chuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titulukire kwa mfumu ya Israele, kapena adzakusungirani moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atumiki ake anamuwuza kuti, “Taonani, ife tamva kuti mafumu a fuko la Israeli ndi achifundo. Tiyeni tipite kwa mfumu ya ku Israeli titavala ziguduli mʼchiwuno mwathu ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwathu. Mwina iye sakakuphani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anyamata ace anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israyeli ndi mafumu acifundo; tiyeni tibvale ciguduli m'cuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titurukire kwa mfumu ya Israyeli, kapena adzakusungirani moyo.