1 Kings 20:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adavaladi ziguduli m'chiwuno ndi kuzeŵeza zingwe m'khosi, napita kwa mfumu ya ku Israele, nkukaiwuza kuti, “Mtumiki wanu Benihadadi akunena kuti, ‘Chonde, mundisungire moyo.’ ” Ahabu adaŵafunsa kuti, “Kani akali moyobe? Iye ujatu ndi mbale wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero anavala chiguduli m'chuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israele, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atavala ziguduli mʼchiwuno mwawo ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwawo, anapita kwa mfumu ya ku Israeli ndipo anayiwuza kuti, “Mtumiki wanu Beni-Hadadi akunena kuti, ‘Chonde loleni kuti ndikhale moyo.’ ” Mfumu inayankha kuti, “Kodi iye akanali ndi moyo? Iye ujatu ndi mʼbale wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero anabvala ciguduli m'cuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israyeli, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga.