1 Kings 20:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthuwo adaganiza kuti mauwo ngabwino, navomera mofulumira kuti, “Inde, Benihadadi ndi mbale wanudi.” Pompo Ahabuyo adati, “Pitani mukamtenge.” Tsono Benihadadi adabweradi ndipo Ahabu adamkweza pa galeta lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono anthuwo anamyang'anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni. Pamenepo Benihadadi anatuluka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m'galeta mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo ankaganiza kuti mawuwo anali abwino ndipo anavomereza mawuwa mofulumira. Iwo anati, “Inde, Beni-Hadadi ndi mʼbale wanu!” Mfumu inati, “Pitani kamutengeni.” Beni-Hadadi atatuluka, Ahabu anamukweza mʼgaleta lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono anthuwo anamyang'anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni, Pamenepo Benihadadi anaturuka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m'gareta mwaceo