1 Kings 20:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Benihadadi adauza Ahabu kuti, “Mizinda imene bambo wanga adalanda bambo wanu ndidzakubwezerani. Tsono mungathe kumanga nyumba zanu zamalonda ku Damasiko, monga momwe adachitira bambo wanga ku Samariya.” Ahabu adamuuza kuti, “Ukachita zimenezi, ndiye kuti ndidzakulola kuti upite.” Tsono adachita naye chipangano, namlola kuti apite.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza midzi ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda m'Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera m'Samariya. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Beni-Hadadi anawuza Ahabu kuti, “Ndidzabweza mizinda imene abambo anga analanda abambo anu. Ndipo mutha kumanga nyumba zanu zamalonda mu Damasiko, monga anachitira abambo anga ku Samariya.” Ahabu anati, “Chifukwa cha mgwirizano umenewu, ine ndidzakumasula.” Choncho anachita naye mgwirizano, ndipo anamulola kuti apite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza midzi ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda m'Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera m'Samaria. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.