1 Kings 20:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mneneri uja adati, “Popeza kuti sudamvere mau a Chauta, ukangochoka pano, mkango ukupha.” Ndiyedi atangochoka pamenepo, adakumana ndi mkango, numupha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena naye, Popeza sunamvera mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha. Ndipo m'mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mneneriyo anati, “Chifukwa sunamvere Yehova, ukangochoka pano, mkango ukupha.” Ndipo munthuyo atangochoka pamenepo, mkango unamupeza ndi kumupha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena naye, Popeza sunamvera mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha, Ndipo m'mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha.