1 Kings 20:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'mene mfumu inkapita pamenepo, mneneri uja adafuula kuti, “Ine mtumiki wanu ndidapita kukailowerera nkhondo pakati penipeni. Ndipo wankhondo wina anabwera kwa ine atatenga mmodzi mwa adani athu, nanena kuti, ‘Sunga munthu uyu. Akasoŵa mwa njira iliyonse, ndiye kuti ndidzakupha kapena udzalipira ndalama 3,000 zasiliva.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popitapo mfumu, anafuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapatuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi chifukwa chilichonse moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, kapena udzalipa talente la siliva,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmene mfumu inkadutsa pamenepo, mneneriyo anafuwula kwa mfumuyo kuti, “Ine mtumiki wanu ndinalowa pakati pa nkhondo, ndipo munthu wina anabwera kwa ine atatenga mmodzi mwa anthu ogwidwa pa nkhondo, nandiwuza kuti, ‘Sunga munthu uyu. Ngati asowa, ndiye kuti ndidzakupha, kapena udzalipira ndalama 3,000 za siliva.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popitapa mfumu, anapfuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapambuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi cifukwa ciri conse moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wace, kapena udzalipa talenti la siliva.