1 Kings 20:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ine mtumiki wanu ndinkatanganidwa apa ndi apa, munthuyo adazemba.” Apo Ahabu, mfumu ya ku Israele, adamuuza kuti, “Momwemo ndimo ukhalire mlandu wako. Iweyo wadzitsutsa wekha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono pochita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israele inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ine mtumiki wanu ndinali wotanganidwa apa ndi apa, munthuyo anasowa.” Mfumu ya Israeli inati, “Chimenechi ndiye chilango chako. Iwe wadziweruza wekha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono pocita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha.