1 Kings 20:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo adachotsa msangamsanga nsalu kumaso, ndipo Ahabu adamzindikira kuti ndi mmodzi mwa aneneri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anafulumira kuchotsa mpango kumaso kwake, ndi mfumu ya Israele inaona kuti anali mmodzi wa aneneri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mneneriyo anachotsa msangamsanga nsalu yomwe anakulunga pa nkhope yake, ndipo mfumu ya Israeli inamuzindikira kuti ndi mmodzi mwa aneneri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anafulumira kucotsa mpango kumaso kwace, ndi mfumu ya Israyeli inaona kuti anali mmodzi wa aneneri.