1 Kings 20:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono amithenga aja adabweranso kwa Ahabu kachiŵiri ndi mau a Benihadadi onena kuti, “Ndidaakuuza kuti unditumizire siliva wako pamodzi ndi golide wako, akazi ako pamodzinso ndi ana ako omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golide wako, ndi akazi ako, ndi ana ako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amithenga aja anabwereranso kwa Ahabu ndipo anamuwuza kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Ine ndinakulamula kuti undipatse siliva wako ndi golide wako, akazi ako ndi ana ako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golidi wako, ndi akazi ako, ndi ana ako;