1 Kings 20:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, ndidzatuma ankhondo anga kumeneko, adzaloŵa m'nyumba zako ndi za nduna zako, ndipo adzatenga zinthu zonse zimene zidzaŵakomere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m'nyumba mwako, ndi m'nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti chifuniro chonse cha maso ako adzachigwira ndi manja ao, nadzachichotsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatuma atumiki anga kudzafufuza mʼnyumba yako yaufumu ndi nyumba za akuluakulu ako. Iwo adzatenga chilichonse chimene umachidalira ndi kupita nacho.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m'nyumba mwako, ndi m'nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti cifuniro conse ca maso ako adzacigwira ndi manja ao, nadzacicotsa.