1 Kings 20:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu Ahabu adaitana akuluakulu onse am'dzikomo naŵauza kuti, “Tsopano mungathe kuwona kuti munthuyu akufuna kutiwononga ife. Adanditumizira mau akuti ndimpatse akazi anga, ana anga, pamodzi ndi siliva ndi golide yemwe, ndipo ine sindidamkanize.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu ya Israele anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti munthu uyu akhumba choipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golide wanga; ndipo sindinamkaniza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mfumu ya Israeli inayitanitsa akuluakulu a mʼdzikomo niwawuza kuti, “Taonani momwe munthuyu akufunira kutibweretsera mavuto! Atatumiza mawu oti ndimupatse akazi anga ndi ana anga, siliva wanga ndi golide wanga, ine sindinamukanize.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu ya Israyeli anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti-munthu uyu akhumba coipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golidi wanga; ndipo sindinamkaniza.