1 Kings 20:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahabuyo adauza amithenga a Benihadadi aja kuti, “Mbuyangayo muuzeni kuti, ‘Zonse zimene adanena poyamba paja ndidzachita zimenezo. Koma zatsopano zokhazi sindingathe kuchita.’ ” Amithenga aja adachoka nakauza Benihadadi mau amenewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba mundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzachita, koma ichi sindingachichite. Nichoka mithengayo, nimbwezera mau.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Ahabu anayankha amithenga a Beni-Hadadi kuti, “Kamuwuzeni mbuye wanga mfumu kuti, ‘Mtumiki wanu adzachita zonse zimene munazifuna nthawi yoyamba ija, koma izi mwazifunazi sindingazikwanitse.’ ” Iwo anachoka nakapereka yankho kwa Beni-Hadadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba kundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzacita, koma ici sindingacicite. Nicoka mithengayo, nimbwezera mau.