1 Kings 21:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero anthu a mumzinda m'mene ankakhala Nabotiyo, akuluakulu ndi atsogoleri amumzindamo, adachitadi monga momwe adaaŵauzira Yezebele. Potsata mau am'makalata omwe mkaziyo adaŵatumizira,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu aja a mudzi wake, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m'mudzi mwake, anachita monga Yezebele anawatumizira, monga munalembedwa m'akalata amene iye anawatumizira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho akuluakulu ndi anthu olemekezeka amene ankakhala ndi Naboti mu mzinda mwake anachita monga analamulira Yezebeli mʼmakalata amene anawalembera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu aja a mudzi wace, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m'mudzi mwace, anacita monga Yezebeli anawatumizira, monga munalembedwa m'akalata amene iye anawatumizira.