1 Kings 21:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aŵiri aja adaloŵa nakhala pamaso pa Nabotiyo. Adayamba akuchita umboni pakhamu pa anthu onse kuti, “Nabotiyu adatemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Motero anthuwo adamtulutsira kunja kwa mzinda, namponya miyala mpaka kumupha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pake, ndipo anthu oipawo anamchitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamtulutsa m'mudzi, namponya miyala, namupha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anthu awiri oyipa anabwera nakhala moyangʼanana naye ndipo anamunenera zoyipa Naboti pamaso pa anthu, ponena kuti, “Naboti watemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Choncho anamutulutsira kunja kwa mzinda ndi kumuponya miyala ndi kumupha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pace, ndipo anthu oipawo anamcitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamturutsa m'mudzi, namponya miyala, namupha.