1 Kings 21:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ukamuuze kuti Chauta akukufunsa kuti, ‘Kodi wapha, ndipo walandanso?’ Ukamuuzenso kuti, ‘Chauta akunena kuti, pa malo amene agalu ankanyambita magazi a Naboti, pomweponso agalu adzanyambita magazi ako.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ukamuwuze kuti: ‘Yehova akuti, Kodi siwapha munthu ndi kumulandanso munda wake?’ Ndipo ukamuwuzenso kuti, ‘Yehova akuti, Pamalo pamene agalu ananyambita magazi a Naboti, pamalo pomwepo agalu adzanyambita magazi ako, inde, akonso!’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, mulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agaru ananyambita mwazi wa Naboti, pompaja agaru adzanyambita mwazi wako, inde wako.