1 Kings 21:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina, Ahabu adauza Naboti kuti, “Tandipatsa munda wakowu kuti ukhale dimba langa, poti uli pafupi ndi nyumba yanga. M'malo mwake ndidzakupatsa wina wabwino koposa, kapena ngati ufuna, ndidzakupatsa ndalama pa mtengo wake wa mundawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, Ndipatse munda wako wamphesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwake ndidzakupatsa munda wamphesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahabu anawuza Naboti kuti, “Patse munda wako wa mpesa kuti ukhale munda wanga wa ndiwo zamasamba, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga yaufumu. Mosinthana ndi mundawu ndidzakupatsa wina wabwino, kapena ngati ungafune, ndidzakupatsa ndalama pa mtengo wake wa mundawu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, diloleni Ndipatse munda wako wamphesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwace ndidzakupatsa munda wamphesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wace,