1 Kings 21:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Ahabu adafunsa Eliya kuti, “Kani wandipeza, iwe mdani wanga?” Eliya adayankha kuti, “Ee, ndakupezani, chifukwa inuyo mwadzigulitsa ndi kukhala ngati kapolo wa zoipa zochimwira Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahabu anati kwa Eliya, “Tsono wandipeza, iwe mdani wanga!” Eliya anayankha kuti, “Inde ndakupezani chifukwa mwadzigulitsa kuti muchite zoyipa pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kucita coipaco pamaso pa Yehova.