1 Kings 21:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo banja lako ndidzalisandutsa kuti likhale ngati banja la Yerobowamu mwana wa Nebati, ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. Nawenso wandikwiyitsa, chifukwa chakuti wachimwitsa anthu a ku Israele’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawononga nyumba yako monga momwe ndinawonongera nyumba ya Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya, chifukwa wandikwiyitsa Ine ndi kuchimwitsa Israeli.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi ya Basa mwana wa Ahiya; cifukwa ca kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kucimwitsa Israyeli.