1 Kings 21:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense wa banja la Ahabu amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Ndipo aliyense wa banja limenelo wodzafera ku thengo, mbalame zamumlengalenga ndizo zidzamudye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwana aliyense wa Ahabu amene adzafera m'mudzi, agalu adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m'mlengalenga zidzamudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Agalu adzadya munthu aliyense wa nyumba ya Ahabu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame za mu mlengalenga zidzadya aliyense wofera ku thengo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwana ali yense wa Ahabu amene adzafera m'mudzi, agaru adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m'mlengalenga zidzamudya,