1 Kings 21:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena zoona kunalibe ndi mmodzi yemwe amene adadzipereka ku zoipa kuchimwira Chauta ngati Ahabu, amene Yezebele mkazi wake adamkopa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Kunalibe munthu ngati Ahabu, amene anadzigulitsa kuchita zoyipa pamaso pa Yehova, amene anakopedwa ndi mkazi wake Yezebeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kucita coipa pamaso pa Yehova, amene Yezebeli mkazi wace anamfulumiza.