1 Kings 21:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga m'mene ankachitira Aamori aja, amene Chauta adaŵachotsa pamene Aisraele ankafika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazichita Aamori, amene Yehova adawapirikitsa pamaso pa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga mmene ankachitira Aamori amene Yehova anawachotsa pamene Aisraeli ankafika).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazicita Aamori, amene Yehova adawapitikitsa pamaso pa ana a Israyeli.