1 Kings 21:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahabu atamva mau amenewo, adang'amba zovala zake, navala ziguduli. Adasala zakudya nagona pa zigudulizo, ndipo adayamba kuyenda modzichepetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zovala zake, navala chiguduli pathupi pake, nasala kudya, nagona pachiguduli, nayenda nyang'anyang'a.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahabu atamva mawu amenewa, anangʼamba zovala zake, navala ziguduli ndi kusala chakudya. Anagona pa ziguduli, nayenda pangʼonopangʼono.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli pathupi pace, nasala kudya, nagona paciguduli, nayenda nyang'anyang'a.