1 Kings 21:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kodi waona m'mene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Popeza kuti wadzichepetsa pamaso panga, sindidzamlanga ndi zonse zija iyeyo ali moyo. Koma ndidzalanga banja lake, kuyambira mwana wake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Chifukwa wadzichepetsa, sindidzabweretsa mavuto amenewa pa nthawi ya moyo wake, koma ndidzawabweretsa pa nyumba yake pa nthawi ya mwana wake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Waona umo wadzicepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzicepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa coipa cimeneci akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wace ndidzacifikitsa pa nyumba yace.