1 Kings 21:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Naboti adauza Ahabu kuti, “Ndithu, pali Chauta, sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Naboti anayankha Ahabu kuti, “Pali Yehova, sindingakupatseni cholowa cha makolo anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni colowa ca makolo anga,