1 Kings 21:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Ahabu adakaloŵa m'nyumba mwake atakwiya, msunamo uli toloo chifukwa cha zimene Naboti wa ku Yezireele adaanena, pakuti adaati, “Sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.” Motero Ahabu adakagona pabedi pake atapenya ku khoma, osafuna ndi kudya komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wake, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Ahabu anapita ku nyumba yake, wachisoni ndi wokwiya chifukwa Naboti wa ku Yezireeli anamuwuza kuti, “Sindidzakupatsani cholowa cha makolo anga.” Ahabu anakagona pa bedi lake atayangʼana kumbali ndipo anakana chakudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwace wamsunamo ndi wokwiya, cifukwa ca mau amene Naboti wa ku Yezreeli adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani colowa ca makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wace, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.