1 Kings 21:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahabu adauza mkazi wakeyo kuti, “Chifukwa chake nchakuti ine ndinakamba ndi Naboti wa ku Yezireele ndi kumuuza kuti andipatse munda wake wamphesawu kuti ndigule, kapena ngati afuna, ndidzamupatse munda wina m'malo mwake. Koma iyeyo wayankha kuti, ‘Sindidzakupatsani munda wanga wamphesawu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati kwa iye, Popeza ndinalankhula kwa Naboti wa ku Yezireele, ndinati kwa iye, Undigulitse munda wako ndi ndalama; kapena ukafuna, ndikupatsa munda wina m'malo mwake; koma anandiyankha, Sindikupatsani munda wanga wamphesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahabu anayankha mkazi wake kuti, “Chifukwa chake nʼchakuti ine ndinamuwuza Naboti wa ku Yezireeli kuti, ‘Gulitse munda wako wa mpesa kapena ngati ungakonde ine ndidzakupatsa munda wina wabwino mʼmalo mwake.’ Koma iye anandiyankha kuti, ‘Sindidzakupatsani munda wanga wa mpesa.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati kwa iye, Popeza ndinalankhula kwa Naboti wa ku Yezreeli, ndinati kwa iye, Undigulitse munda wako ndi ndalama; kapena ukafuna, ndikupatsa munda wina m'malo mwace; kama anandiyankha, Sindikupatsani munda wanga wamphesa.