1 Kings 21:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yezebele mkazi wakeyo adamufunsa kuti, “Kodi mfumu ya ku Israele sindinu? Dzukani, kadyeni, mtima wanu usangalale. Ine ndidzakutengerani munda wamphesawo kwa Naboti wa ku Yezireele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yezebele mkazi wake anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisraele tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezireele ndidzakupatsani ndine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yezebeli mkazi wake anati, “Kodi umu ndi mmene mumachitira ngati mfumu ya Israeli? Dzukani, idyani! Sangalalani. Ine ndidzakutengerani munda wamphesa wa Naboti wa ku Yezireeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yezebeli mkazi wace anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisrayeli tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezreeli ndidzakupatsani ndine.