1 Kings 21:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yezebele adalemba makalata m'dzina la Ahabu, naŵasindikiza ndi chidindo cha mfumu. Adatumiza makalatawo kwa akuluakulu ndi kwa atsogoleri amene ankakhala ndi Naboti mumzinda mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo analemba akalata m'dzina la Ahabu nakhomerapo chizindikiro chake, natumiza akalatawo kwa akulu ndi omveka anali m'mudzi mwake, nakhala naye, Naboti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yezebeli analemba makalata mʼdzina la Ahabu, nawadinda chidindo cha mfumu, nawatumiza makalatawo kwa akuluakulu ndi kwa anthu olemekezeka amene ankakhala ndi Naboti mu mzinda mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo analemba akalata m'dzina la Ahabu nakhomerapo cizindikilo cace, natumiza akalatawo kwa akulu ndi omveka anali m'mudzi mwace, nakhala naye Naboti.