1 Kings 22:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adaakhala pa mipando yao yaufumu, atavala zovala zao zaufumu. Pamenepo panali pa bwalo lopererapo tirigu, pa khomo la pa chipata cha Samariya. Ndipo aneneri onse ankalosa pamaso pa mafumuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zao zachifumu pabwalo popondera mphesa pa khomo la chipata cha Samariya; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atavala mikanjo yawo yaufumu, mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopondera tirigu pafupi ndi chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wacifumu wace, obvala zobvala zao zacifumu pabwalo pa khomo la cipata ca Samaria; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.