1 Kings 22:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina mwa iwo, Zedeki, mwana wa Kenana adaadzisulira nyanga zachitsulo. Iyeyo adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndi nyangazi iwe udzagonjetsa Asiriya mpaka kuŵaonongeratu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana nʼkuti atapanga nyanga zachitsulo ndipo iye ananenera kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi, inu mudzagunda nazo Aaramu mpaka iwo atawonongeka.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zacitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti,