1 Kings 22:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wamthenga uja amene adaapita kukaitana Mikaya namuuza kuti, “Onani, mau onse amene akunena aneneri, akulosera mfumu zabwino. Ndiye nanunso mau anu akhale ofanafana ndi mau aowo. Muzilosa zabwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri avomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa mmodzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wamthenga amene anapita kukayitana Mikaya anamuwuza kuti, “Taonani, aneneri onse monga munthu mmodzi akunenera za kupambana kwa mfumu. Mawu anunso akhale ogwirizana ndi mawu awo, ndipo mukayankhule zabwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri abvomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa m'modzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.