1 Kings 22:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atafika kwa Ahabu, mfumuyo idamfunsa kuti, “Kodi Mikaya, ife tipite kukamenya nkhondo ku Ramoti-Giliyadi, kapena tileke?” Iye adayankha kuti, “Pitani, mukapambana. Chauta adzaupereka mzindawo kwa inu amfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Giliyadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzachita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika, Ahabu anamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena tileke?” Iye anayankha kuti, “Pitani ndipo mukapambana, pakuti Yehova adzawupereka mzindawo mʼdzanja la mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Gileadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzacita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.