1 Kings 22:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mikaya adati, “Ndidaona Aisraele onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono Chauta adati, ‘Ameneŵa alibe mbuyawo. Aliyense apite kwao mwamtendere.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi zilibe mwini, yense abwerere ndi mtendere kunyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Mikaya anayankha kuti, “Ndinaona Aisraeli onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mwamtendere.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Ndinaona Aisrayeli onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi ziribe mwini, yense abwerere ndi mtendere ku nyumba yace.