1 Kings 22:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mikaya adati, “Nchifukwa chake mverani mau a Chauta. Ine ndidapenya Chauta atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse lakumwamba litaima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mikaya anapitiriza kuyankhula nati, “Tsono imvani mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse la kumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Cifukwa cace tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wace wacifumu, ndi khamu lonse la Kumwamba liri ciriri m'mbali mwace, ku dzanja lamanja ndi lamanzere,