1 Kings 22:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mikaya adati, “Mukabwerera mwamtendere, ndiye kuti Chauta sadalankhule kudzera mwa ine.” Ndipo adaonjeza kuti, “Mumve anthu nonsenu zimene ndanenazi!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mikaya ananena kuti, “Ngati mudzabwerera mwamtendere, Yehova sanayankhule kudzera mwa ine.” Ndipo iye anapitiriza kunena kuti, “Gwiritsitsani mawu angawa, anthu inu nonse!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhula mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.