1 Kings 22:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahabu adafunsa aphungu ake kuti, “Ramoti-Giliyadi ndi mzinda wathu, nanga chifukwa chiyani ife tikukhala chete, osaulanda kwa mfumu ya ku Siriya?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Israele ananena ndi anyamata ake, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Giliyadi ngwathu, ndipo tangokhala chete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya ku Israeli nʼkuti itawuza atumiki ake kuti, “Kodi inu simukudziwa kuti Ramoti Giliyadi ndi dera lathu ndipo ife palibe chimene tikuchita kuti tilitenge deralo mʼmanja mwa mfumu ya Aramu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Israyeli ananena ndi anyamata ace, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Gileadi ngwathu, ndipo tangokhala cete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu.