1 Kings 22:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Ine ndidzizimbaitsa, ndipo ndipita kunkhondoko, koma iwe uvale malaya ako aufumu.” Choncho mfumu ya ku Israele idadzizimbayitsa onsewo nkupita ku nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulowa kunkhondo, koma vala iwe zovala zako zachifumu. Ndipo mfumu ya Israele inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya ku Israeli inawuza Yehosafati kuti, “Ine ndidzalowa mu nkhondoyi modzibisa, koma inu muvale zovala zanu zaufumu.” Choncho mfumu ya ku Israeli inadzibisa ndi kupita ku nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Israyeli inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulawa kunkhondo, koma bvala iwe zobvala zako zacifumu. Ndipo mfumu ya Israyeli inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.