1 Kings 22:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Siriya nkuti italamula akapitao a magaleta okwanira 32, kuti asamenye nkhondo ndi wina aliyense, wamng'ono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israele basi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magaleta ake, niti, Musaponyana ndi anthu ang'ono kapena akulu, koma ndi mfumu ya Israele yokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mfumu ya ku Aramu nʼkuti italamulira anthu ake 32 olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magareta ace, niti, Musaponyana ndi anthu ang'ono kapena akuru, koma ndi mfumu ya Israyeli yokha.