1 Kings 22:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene akapitao a magaletawo adaona Yehosafati, adati, “Ndithudi ameneyo ndiye mfumu ya ku Israele.” Choncho adabwerera kudzalimbana naye. Yehosafati adayamba kufuula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, akapitao a magaleta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israele imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anafuula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Olamulira magaleta ataona Yehosafati, ankaganiza kuti, “Ndithu iyi ndiye mfumu ya ku Israeli.” Choncho anabwerera kukamenyana naye, koma Yehosafati atafuwula,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, akapitao a magareta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israyeli imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anapfuula.