1 Kings 22:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Msiriya wina adakoka uta wake mwachiponyeponye, ndipo adalasa mfumu ya ku Israele pa maluma a malaya ake achitsulo. Pamenepo mfumuyo idauza munthu woyendetsa galeta lake kuti, “Tembenuka, ndipo undichotse pankhondo pano poti ndavulazidwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu anakoka uta wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israele pakati pa maluma a malaya achitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa galeta wake, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndi kulasa mfumu ya ku Israeli polumikizira malaya ake odzitetezera. Mfumu inawuza woyendetsa galeta lake kuti, “Tembenuka ndipo undichotse pa nkhondo pano pakuti ndalasidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu anakoka uta wace ciponyeponye, nalasa mfumu ya Israyeli pakati pa maluma a maraya acitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa gareta wace, Tembenuza dzanja lako, nundicotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.