1 Kings 22:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhondo idakula kwambiri tsiku limenelo, mwakuti mfumu ija adangoisiya ili tsonga m'galeta lake atayang'anana ndi Asiriya, mpaka mfumuyo idafa madzulo. Monsemo nkuti magazi akutayikira pansi pa galetalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nkhondo inakula tsiku lomwelo, ndipo mfumu inagwirizidwa m'galeta mwake kupenyana ndi Aaramu, natsirizika madzulo; ndipo mwazi unatuluka m'bala pa phaka la galeta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nkhondo inakula kwambiri tsiku limenelo, ndipo mfumu inakhala tsonga mʼgaleta lake moyangʼanana ndi Aaramu. Magazi ake ankayenderera pansi kuchokera mʼgaleta, ndipo pa nthawi ya madzulo inamwalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nkhondo inakula tsiku lomwelo, ndipo mfumu inagwirizidwa m'gareta mwace kupenyana ndi Aaramu, natsirizika madzulo; ndipo mwazi unaturuka m'bala pa phaka la gareta.