1 Kings 22:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja adatsuka galeta lija ku chidziŵe cha ku Samariya, kumene akazi adama ankasamba. Ndipo agalu adayamba kunyambita magazi a mfumuyo, potsata mau amene Chauta adaalankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo potsuka galetayo pa thawale la ku Samariya agalu ananyambita mwazi wake, paja pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatsuka galeta lija pa dziwe la ku Samariya (pamene ankasamba akazi achiwerewere) ndipo agalu ananyambita magazi a mfumuyo, monga momwe Yehova ananenera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo potsuka garetayo pa thawale la ku Samaria agaru ananyambita mwazi wace, pala pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo.