1 Kings 22:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zina za Ahabu ndi zonse zimene adazichita, kudzanso za nyumba ya minyanga ya njovu yomwe adaimanga, ndiponso za mizinda yonse imene adaimanga, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono machitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazichita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi midzi yonse adaimanga, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ntchito zina za Ahabu, kuphatikiza zonse anazichita, nyumba yaufumu imene anamanga yokutidwa ndi minyanga ya njovu, mizinda yotetezedwa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono macitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazicita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi midzi yonse adaimanga, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?