1 Kings 22:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane limodzi ku nkhondo ku Ramoti-Giliyadi?” Yehosafati adauza mfumu ya ku Israeleyo kuti, “Ine ndili nanu limodzi, anthu anga nganu, akavalo anga nganunso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Giliyadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavalo ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iye anafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane ku nkhondo ku Ramoti Giliyadi?” Yehosafati anayankha mfumu ya ku Israeli kuti, “Ine ndili monga inu, anthu anga monga anthu anu, akavalo anga monga akavalo anu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Gileadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israyeli, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavale ako.