1 Kings 22:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yehosafati ankayenda motsata chitsanzo chabwino cha atate ake. Sadapatuke pa zimenezo. Ankachita zolungama pamaso pa Chauta. Komabe akachisi opembedzerako mafano sadaŵawononge, mwakuti anthu ankaperekabe nsembe ndipo ankafukizabe lubani pa malowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wake Asa, osapatukamo; nachita choyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa zinthu zonse, Yehosafati anayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanachite zotsutsana ndi machitidwe a abambo ake. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova. Komabe, malo azipembedzo sanawawononge, ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wace Asa, osapambukamo; nacita coyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaicotsa; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.