1 Kings 22:45 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zina zonse za Yehosafati, mphamvu zimene adaonetsa, ndiponso maponyedwe ake a nkhondo, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono machitidwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito zake zina za Yehosafati, zinthu zimene anachita ndi zamphamvu zimene anaonetsa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Yuda?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono maciddwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?